Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 3:17-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Ndipo mkazi mmodzi anati, Mbuye wanga, ine ndi mkazi uyu tikhala awiri m'nyumba imodzi; ndipo ine ndinaona mwana, iye ali m'nyumbamo.

18. Ndipo kunacitika kuti tsiku lacitatu nditaona ine mwana, mnzangayu anaonanso mwana; ndipo ife tinali pamodzi, munalibe mlendo ndi ife m'nyumbamo, koma ife awiri m'nyumbamo.

19. Ndipo mwana wa mnzangayu anamwalira usiku, pokhala iyeyu anamgonera.

20. Ndipo iye anauka pakati pa usiku, natenga mwana wanga kumimba kwanga, mdzakazi wanu ndiri m'tulo, namuika m'mfukato mwace, naika mwana wace wakufa m'mfukato mwanga.

21. Ndipo pouka ine m'mawa kuyamwitsa mwana wanga ndaona ngwakufa, koma nditamzindikira m'mawa ndaona si mwana wanga wobala ine ai.

22. Ndipo mkazi winayo anati, lai, koma wamoyoyu ndi mwana wanga, ndi wakufayu ndi mwana wako. Ndipo uja anati, lai, koma wakufayu ndi mwana wako, ndi wamoyoyu ndi mwana wanga. Motero iwo analankhula pamaso pa mfumu.

23. Tsono mfumu inati, Uyu akuti, Wamoyoyu ndiye mwana wanga ndi wakufayu ndiye mwana wako; ndipo winayo akuti, lai, koma mwana wako ndiye wakufayu, ndi mwana wanga ndiye wamoyoyu.

24. Niti mfumu, Kanaitengereni cimpeni. Ndipo iwo anabwera ndi cimpeni kwa mfumu.

25. Mfumu niti, Dula pakati mwana wamoyoyu, nupatse mmodzi cipinjiri, ndi wina cipinjiri cace.

26. Koma mkazi amene mwana wamoyo anali wace analankhula ndi mfumu, popeza mtima wace unalira mwana wace, nati, Ha! mbuye wanga, mumpatse uyo mwana wamoyo osamupha konse. Koma winayo anati, Asakhale wanga kapena wako, dulani.

27. Pamenepo mfumu inayankha, niti, Mumpatse wacifundoyo mwana wamoyo, osamupha konse, uyo ndiye amace.

28. Ndipo Aisrayeli onse anamva maweruzidwe ace idaweruza mfumu, naopa mfumu; pokhala anaona kuti nzeru ya Mulungu inali mwa iye yakuweruza.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 3