Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 22:34-50 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

34. Ndipo munthu anakoka uta wace ciponyeponye, nalasa mfumu ya Israyeli pakati pa maluma a maraya acitsulo; tsono ananena ndi mnyamata wa gareta wace, Tembenuza dzanja lako, nundicotse kunkhondo, popeza ndalasidwa.

35. Ndipo nkhondo inakula tsiku lomwelo, ndipo mfumu inagwirizidwa m'gareta mwace kupenyana ndi Aaramu, natsirizika madzulo; ndipo mwazi unaturuka m'bala pa phaka la gareta.

36. Ndipo mfuu unafikira khamu lonse la nkhondo polowa dzuwa, ndi kuti, Yense kumudzi kwao, ndi yense ku dziko la kwao.

37. Ndipo inafa mfumu, naifikitsa ku Samaria, naika mfumu m'Samaria.

38. Ndipo potsuka garetayo pa thawale la ku Samaria agaru ananyambita mwazi wace, pala pamasamba akazi adama, monga mwa mau a Yehova amene ananenawo.

39. Tsono macitidwe ena a Ahabu, ndi zonse adazicita, ndi nyumba ya minyanga adaimanga, ndi midzi yonse adaimanga, kodi sizilembedwa m'buku la macitidwe a mafumu a Israyeli?

40. Ndipo Ahabu anagona ndi makolo ace; ndi Ahaziya mwana wace anakhala mfumu m'malo mwace.

41. Koma Yehosafati mwana wa Asa anayamba kukhala mfumu ya Yuda caka cacinai ca Ahabu mfumu ya Israyeli.

42. Yehosafati anali wa zaka makumi atatu mphambu zisanu, pamene analowa ufumu, nakhala nifumu zaka makumi awiri mphambu zisanu m'Yerusalemu. Ndi dzina la amace linali Azuba mwana wa Sili.

43. Ndipo anayenda m'njira yonse ya atate wace Asa, osapambukamo; nacita coyenera pamaso pa Yehova, koma misanje sanaicotsa; anthu anapherabe nsembe, nafukiza zonunkhira pamsanje.

44. Ndipo Yehosafati anacitana mtendere ndi mfumu ya Israyeli.

45. Tsono maciddwe ena a Yehosafati, ndi mphamvu anaionetsayo, ndi umo anathira nkhondo, kodi sizilembedwa m'buku la macitidwe a mafumu a Yuda?

46. Ndipo anacotsa m'dziko anyamata onyansa aja adatsalira masiku a atate wace Asa.

47. Ndipo m'Edomu munalibe mfumu, koma kazembe wa mfumu.

48. Yehosafati anamanga zombo za ku Tarsisi kukatenga golidi ku Ofiri; koma sizinamuka, popeza zinaphwanyika pa Ezioni Geberi.

49. Pamenepo Ahaziyamwana wa Ahabu ananena ndi Yehosafati, Anyamata anga amuke pamodzi ndi anyamata anu m'zombo. Koma Yehosafati anakana.

50. Ndipo Yehosafati anagona ndi makolo ace, naikidwa ndi makolo ace m'mudzi wa Davide kholo lace; ndipo Yoramu mwana wace anakhala mfumu m'malo mwace.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 22