Ndipo munthu anakoka uta wace ciponyeponye, nalasa mfumu ya Israyeli pakati pa maluma a maraya acitsulo; tsono ananena ndi mnyamata wa gareta wace, Tembenuza dzanja lako, nundicotse kunkhondo, popeza ndalasidwa.