Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 2:36-44 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

36. Ndipo mfumu inatuma munthu kukaitana Simeyi, nati kwa iye, Udzimangire nyumba m'Yerusalemu, nukhale komweko osaturukako kumka kwina konse.

37. Popeza tsiku lomwelo lakuturuka iwe ndi kuoloka mtsinje Kidroni, tadziwa ndithu kuti udzafadi, mwazi wako udzakhala pa mutu wa iwe wekha.

38. Ndipo Simeyi ananena ndi mfumu, Mau awa ndi abwino; monga momwe mwanena mbuye wanga mfumu momwemo ndidzacita kapolo wanu. Ndipo Simeyi anakhala m'Yerusalemu masiku ambiri.

39. Ndipo kunacitika, zitapita zaka zitatu, kuti akapolo awiri a Simeyi anathawira kwa Akisi mwana wa Maaka mfumu ya Gati. Ndipo anamuuza Simeyi, nati, Taonani, akapolo anu akhala ku Gati.

40. Ndipo Simeyi ananyamuka, namangirira mbereko pa buru wace, namka ku Gati kwa Akisi kukafuna aka polo ace; namuka Simeyi, nabwera nao akapolo ace kucokera ku Gati.

41. Ndipo anamuuza Solomo, kuti, Simeyi wacoka ku Yerusalemu kumka ku Gati, nabweranso.

42. Ndipo mfumu inatuma munthu kukaitana Simeyi, niti kwa iye, Kodi sindinakulumbiritsa pa Yehova ndi kukucenjeza, kuti, Tadziwa ndithu, kuti tsiku lakuturuka iwe ndi kukayenda kwina konse udzafa ndithu? Ndipo iwe unati kwa ine, Mau amene ndawamva ndi abwino.

43. Sunasunga cifukwa ninji lumbiro la pa Yehova, ndi lamulo lija ndinakulamulira iwe?

44. Tsono mfumu inanenanso ndi Simeyi, Udziwa iwe coipa conse mtima wako umadziwaco, cimene udacitira Davide atate wanga; cifukwa cace Yehova adzakubwezera coipa cako pamutu pako mwini.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 2