Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 2:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pakuyandikira masiku ace a Davide akuti amwalire, analamulira Solomo mwana wace, nati,

2. Ndimuka ine njira ya dziko lonse: limba mtima tsono, nudzionetse umunthu;

3. nusunge cilangizo ca Yehova Mulungu wako, kuyenda m'njira zace, kusunga malemba ndi malamulo ndi maweruzo ndi umboni wace, monga mulembedwa m'cilamulo ca Mose, kuti ukacite mwa nzeru m'zonse ukacitazo, ndi kumene konse ukatembenukirako;

4. kuti Yehova akakhazikitse mau ace adanenawo za ine, kuti, Ngati ana ako akasunga bwino njira zao, kuyenda moona pamaso pa Ine ndi mtima wao wonse ndi moyo wao wonse, nditi sipadzakusowa mwamuna mmodzi pa mpando wacifumu wa Israyeli.

5. Ndiponso udziwa cimene Yoabu mwana wa Zeruya anandicitira, inde cimene anawacitira akazembe awiri aja a magulu a nkhondo a Israyeli, ndiwo Abineri mwana wa Neri, ndi Amasa mwana wa Yeteri, amene aja anawapha, nakhetsa mwazi ngati wa nkhondo masiku a mtendere, napaka mwazi wa nkhondo pa lamba lace la m'cuuno mwace, ndi pa nsapato za pa mapazi ace.

6. Cita mwa nzeru yako tsono, osalola mutu wace waimvi utsikire kumanda ndi mtendere.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 2