Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 18:16-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Ndipo Obadiya anauka kukomana ndi Ahabu, namuuza, ndipo Ahabu ananka kukomana ndi Eliya.

17. Ndipo kunacitika pamene Ahabu anaona Eliya, Ahabu anati kwa iye Kodi ndiwe uja umbvuta Israyeliyo?

18. Nati iye, Sindimabvuta Israyeli ine ai, koma inu ndi nyumba ya atate wanu; popeza munasiya malamulo a Yehova, ndi kutsata Abaala.

19. Ndipo tsono, tumani mundimemezere Aisrayeli onse ku phiri la Karimeli, ndi aneneri a Baala mazana anai mphambu makumi asanu, ndi aneneri a cifanizoco mazana anai, akudya pa gome la Yezebeli.

20. Pamenepo Ahabu anatumiza mau kwa ana onse a Israyeli, namemeza aneneri onse ku phiri la Karimeli.

21. Ndipo Eliya anayandikira kwa anthu onse, nati, Mukayika-kayika kufikira liti? ngati Yehova ndiye Mulungu, mtsateni iye; ngati Baala, mumtsate iyeyo. Ndipo anthu nnena kumyankha mau amodzi.

22. Ndipo Eliya ananena ndi anthuwo, Ine ndatsala ndekha mneneri wa Yehova, koma aneneri a Baala ndiwo anthu mazana anai mphambu makumi asanu.

23. Atipatse tsono ng'ombe ziwiri; ndipo adzisankhire iwo eni ng'ombe imodzi, naiduledule, naiike pankhuni osasonkhapo moto; ndipo ine ndidzakonza ng'ombe yinayo, ndi kulika pankhuni osasonkhapo moto.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 18