Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 18:13-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Kodi sanakuuzani mbuye wanga cimene ndidacita m'kuwapha Yezebeli aneneri a Yehova, kuti ine ndidabisa aneneri a Yehova zana limodzi makumi asanu asanu m'phanga, ndikuwadyetsa mkate ndi madzi?

14. Ndipo tsopano inu mukuti, Kauze mbuye wako Eliya wabwera, ndipo adzandipha.

15. Koma Eliya anati, Pali Yehova wa makamu, amene ndikhala pamaso pace, zedi, ndionekadi pamaso pace lero.

16. Ndipo Obadiya anauka kukomana ndi Ahabu, namuuza, ndipo Ahabu ananka kukomana ndi Eliya.

17. Ndipo kunacitika pamene Ahabu anaona Eliya, Ahabu anati kwa iye Kodi ndiwe uja umbvuta Israyeliyo?

18. Nati iye, Sindimabvuta Israyeli ine ai, koma inu ndi nyumba ya atate wanu; popeza munasiya malamulo a Yehova, ndi kutsata Abaala.

19. Ndipo tsono, tumani mundimemezere Aisrayeli onse ku phiri la Karimeli, ndi aneneri a Baala mazana anai mphambu makumi asanu, ndi aneneri a cifanizoco mazana anai, akudya pa gome la Yezebeli.

20. Pamenepo Ahabu anatumiza mau kwa ana onse a Israyeli, namemeza aneneri onse ku phiri la Karimeli.

21. Ndipo Eliya anayandikira kwa anthu onse, nati, Mukayika-kayika kufikira liti? ngati Yehova ndiye Mulungu, mtsateni iye; ngati Baala, mumtsate iyeyo. Ndipo anthu nnena kumyankha mau amodzi.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 18