Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 16:11-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Ndipo kunali, atalowa ufumu wace, nakhala pa mpando wacifumu wace, anawakantha onse a m'nyumba ya Basa, osamsiyira mwana wamwamuna ndi mmodzi yense, kapena wa abale ace, kapena wa mabwenzi ace.

12. Motero Zimri anaononga nyumba yonse ya Basa, monga mwa mau a Yehova, amene ananena akumtsutsa Basa, mwa dzanja la Yehu mneneri,

13. cifukwa ca macimo onse a Basa, ndi macimo a Ela mwana wace anacimwawo, nacimwitsa nao Aisrayeli, kuputa mkwiyo wa Yehova Mulungu wa Israyeli ndi zacabe zao.

14. Tsono macitidwe ena a Ela, ndi nchito zace zonse, kodi sizilembedwa m'buku la macitidwe a mafumu a Israyeli?

15. Ndipo caka ca makumi awiri mphambu zisanu ndi ziwiri ca Asa mfumu ya Yuda, Zimri anali mfumu masiku asanu ndi awiri ku Tiriza. Ndipo anthu analikumangira misasa Gibetoni wa Afilisti.

16. Koma anthu aja omangira misasa anamva kuti Zimri wacita ciwembu, nakanthanso mfumu; cifukwa cace tsiku lomwelo Aisrayeli onse a kumisasa anamlonga Omri kazembe wa nkhondo akhale mfumu ya Israyeli.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 16