Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 15:24-32 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

24. Nagona Asa ndi makolo ace, naikidwa kwa makolo ace m'mudzi wa Davide kholo lace; ndipo Yosafati mwana wace analowa ufumu m'malo mwace.

25. Ndipo Nadabu mwana wa Yerobiamu analowa ufumu wa Israyeli caka caciwiri ca Asa mfumu ya Yuda, nakhala mfumu ya Israyeli zaka ziwiri.

26. Nacita zoipa pamaso pa Yehova, nayenda m'njira ya atate wace, ndi m'chimo lomwelo iye akacimwitsa nalo Aisrayeli.

27. Ndipo Basa mwana wa Akiya, wa nyumba ya Isakara, anampangira ciwembu; ndipo Basa anamkanthira ku Gibetoni wa Afilisti, popeza Nadabu ndi Aisrayeli onse adamangira misasa Gibetoni.

28. Inde Basa anamupha caka cacitatu ca Asa mfumu ya Yuda, nalowa ufumu m'malo mwace.

29. Tsonokunacitika, pokhalamfumu iye, anakantha nyumba yonse ya Yerobiamu, osasiyako wamoyo ndi mmodzi yense wa Yerobiamu, kufikira adamuononga monga mwa mau a Yehova, amene analankhula pa dzanja la mtumiki wace Ahiya wa ku Silo;

30. cifukwa ca macimo a Yerobiamu, amene adacimwa nao, nacimwitsa nao Aisrayeli, ndi kuutsa kwace kumene anaputa nako mkwiyo wa Yehova Mulungu wa Israyeli.

31. Ndipo macitidwe ena a Nadabu, ndi zonse anazicita, kodi sizilembedwa m'buku la macitidwe a mafumu a Israyeli?

32. Ndipo panali nkhondo pakati pa Asa ndi Basa mfumu ya Israyeli masiku ao onse.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 15