21. Tsono Basa atamva izi, analeka kumanga ku Rama nakhala pa Tiriza.
22. Pamenepo mfumu Asa anamemeza Ayuda onse, osatsala ndi mmodzi yense; natuta miyala ya ku Rama, ndi mitengo yomwe, akamange nayo Basa; ndi mfumu Asa anamangira Geba wa ku Benjamini, ndi Mizipa.
23. Ndipo macitidwe onse ena a Asa, ndi mphamvu yace yonse, ndi zonse anazicita, ndi midzi anaimanga, kodi sizilembedwa m'buku la macitidwe a mafumu a Yuda? Koma masiku a ukalamba wace anadwala mapazi ace.
24. Nagona Asa ndi makolo ace, naikidwa kwa makolo ace m'mudzi wa Davide kholo lace; ndipo Yosafati mwana wace analowa ufumu m'malo mwace.