Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 1:46-53 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

46. Ndiponso Solomo wakhala pa cimpando ca ufumu.

47. Ndiponso akapolo a mfumu anadzadalitsa Davide mbuye wathu mfumu, nati, Mulungu wanu aposetse dzina la Solomo lipunde dzina lanu, nakulitse mpando wace wacifumu upose mpando wanu wacifumu; ndipo mfumu anawerama pakamapo.

48. Ndiponso watero mfumu, Wolemekezeka Yehova Mulungu wa Israyeli, amene wapereka lero wina wokhala pa mpando wanga wacifumu, maso anga ali cipenyere.

49. Pamenepo oitanidwa onse a Adoniya anacita mantha, nanyamuka, napita yense njira yace.

50. Ndipo Adoniya anaopa cifukwa ca Solomo, nanyamuka, nakagwira nyanga za guwa la nsembe.

51. Ndipo anthu anakauza Solomo, kuti, Taonani, Adoniya aopa mfumu Solomo, popeza taonani, wagwira nyanga za guwa la nsembe, nati, Mfumu Solomo alumbirire ine lero kuti sadzandipha kapolo wace ndi lupanga.

52. Ndipo Solomo anati, iye akakhala munthu woyenera silidzagwa pansi tsitsi lace limodzi lonse; koma mukapezeka mwa iye coipa, adzafadi.

53. Tsono mfumu Solomo anatuma anthu nakamtsitsa ku guwa la nsembe. Iye nadza, nagwadira mfumu Solomo; Solomo nati kwa iye, Pita kwanu.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 1