Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 1:34-39 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

34. Ndipo Zadoki wansembe ndi Natani mneneri akamdzoze kumeneko akhale mfumu ya Israyeli; ndipo muombe lipenga, ndi kuti, Mfumu Solomo akhale ndi moyo.

35. Pamenepo mumtsate iye, iye nadzadza nadzakhala pa mpando wanga wacifumu, popeza adzakhala iyeyu mfumu m'malo mwanga; ndipo ndamuika iye akhale mtsogoleri wa lsrayeli ndi Yuda.

36. Ndipo Benaya mwana wa Yehoyada anayankha mfumu, nati, Amen, ateronso Yehova Mulungu wa mbuye wanga mfumu.

37. Monga umo Yehova anakhalira ndi mbuye wanga mfumu, momwemo akhalenso ndi Solomo, nakuze mpando wace wacifumu upose mpando wacifumu wa mbuye wanga mfumu Davide.

38. Pamenepo Zadoki wansembe, ndi Natani mneneri, ndi Benaya mwana wa Yehoyada, ndi Akereti, ndi Apeleti aja anatsika, nakweza Solomo pa nyuru ya mfumu Davide, nafika naye ku Gihoni.

39. Ndipo Zadoki wansembe anatenga nyanga ya mafuta inali m'Cihema, namdzoza Solomo. Ndipo iwo anaomba lipenga, ndi anthu onse anati, Mfumu Solomo akhale ndi moyo.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 1