3. ndi pacidikha mpaka nyanja ya Kineroti kum'mawa, ndi mpaka nyanja ya kucidikha, ndiyo Nyanja ya Mcere kum'mawa, njira ya Beti-Yesimoti; ndi kumwela pansi pa matsikiro a Pisiga.
4. Nalandanso malire a Ogi mfumu ya Basana wotsala wa Arefai, wokhala ku Asitarotu ndi ku Edrei,
5. nacita ufumu m'phiri la Herimoni, ndi m'Saleka, ndi m'Basana lonse, mpaka malire a Agesuri, ndi a Maakati, ndi Gileadi wogawika pakati, malire a Sihoni mfumu ya ku Hesiboni.
6. Mose mtumiki wa Yehova ndi ana a Israyeli anawakantha; ndi Mose mtumiki wa Yehova analipereka kwa Arubeni, ndi Agadi ndi pfuko la Manase logawika pakati, likhale colowacao.
7. Ndipo awa ndi mafumu a dzikolo amene Yoswa ndi ana a Israyeli anawakantha tsidya lija la Yordano kumadzulo, kuyambira Baala-gadi m'cigwa ca Lebano mpaka phiri la Halaki lokwera kumka ku Seiri; ndipo Yoswa analipereka kwa mapfuko a Israyeli, likhale lao lao, monga mwa magawo ao;
8. kumapiri ndi kucigwa, ndi kucidikha, ndi kumatsikiro, ndi kucipululu, ndi kumwela: Ahiti, Aamori, ndi Akanani, Aperizi, Ahivi ndi Ayebusi:
9. mfumu ya ku Yeriko, imodzi; mfumu ya ku Ai, ndiwo m'mbali mwa Beteli, imodzi;
10. mfumu ya ku Yerusalemu, imodzi; mfumu ya ku Hebroni, imodzi; mfumu ya ku Yarimutu, imodzi;
11. mfumu ya ku Lakisi, imodzi;
12. mfumu ya ku Egiloni, imodzi; mfumu ya ku Gezere, imodzi;
13. mfumu ya ku Dibiri, imodzi; mfumu ya ku Gederi, imodzi;
14. mfumu ya ku Horima, imodzi; mfumu ya ku Haradi, imodzi;