11. momwemo adzakhala mau anga amene aturuka m'kamwa mwanga, sadzabwerera kwa Ine cabe, koma adzacita cimene ndifuna, ndipo adzakula m'mene ndinawatumizira.
12. Pakuti inu mudzaturuka ndi kukondwa, ndi kutsogozedwa ndi mtendere; mapiri ndi zitunda, zidzayimba zolimba pamaso panu, ndi mitengo yonse ya m'thengo idzaomba m'manja mwao.
13. M'malo mwa mithethe mudzaturuka mtengo wamlombwa; ndi m'malo mwa lunguzi mudzamera mtengo wamcisu; ndipo cidzakhala kwa Yehova ngati mbiri, ngati cizindikiro cosatha, cimene sicidzalikhidwa.