11. Ndipo oomboledwa a Yehova adzabwera, nadzafika ku Ziyoni; ndi nyimbo ndi kukondwa kosatha kudzakhala pa mitu yao; adzakhala m'kusangalala ndi kukondwa, ndipo cisoni ndi kuusa moyo kudzacoka.
12. Ine, Inedi, ndine amene nditonthoza mtima wako; kodi iwe ndani, kuti uopa munthu amene adzafa, ndi mwana wa munthu amene adzakhala ngati udzu;
13. waiwala Yehova Mlengi wako, amene anayala m'mwamba, nakhazika maziko a dziko lapansi, ndi kuopabe tsiku lonse cifukwa ca ukali wa wotsendereza, pamene iye akonzeratu kupasula? uli kuti ukali wa wotsendereza?
14. Wam'nsinga wowerama adzamasulidwa posacedwa; sadzafa ndi kutsikira kudzenje, cakudya cace sicidzasowa.
15. Pakuti Ine ndine Yehova Mulungu wako, amene ndiutsa nyanja, kuti mafunde ace akokome; Yehova wa makamu ndi dzina lace.
16. Ndipo ndaika mau anga m'kamwa mwako; ndipo ndakuphimba ndi mthunzi wa dzanja langa, kuti ndikhazike kumwamba ndi kuika maziko a dziko lapansi, ndi kunena kwa Ziyoni, Inu ndinu anthu anga.
17. Galamuka, galamuka, imirira Yerusalemu amene unamwa m'dzanja la Yehova cikho ca ukali wace; iwe wamwa mbale ya cikho conjenjemeretsa ndi kucigugudiza.
18. Palibenso wina wakumtsogolera mwa ana amuna onse, amene iye anawabala; palibe wina amgwira dzanja mwa ana onse anawalera.
19. Izi ziwiri zakugwera; ndani adzakulira iwe? bwinja ndi cipasuko, njala ndi lupanga; ndidzatonthoza mtima wako bwanji?
20. Ana ako amuna akomoka; agona pamtu pa makwalala onse, monga nswala muukonde; adzala ndi ukali wa Yehova, kudzudzula kwa Mulungu wako,
21. Cifukwa cace imva ici tsopano, iwe wobvutidwa ndi woledzera koma si ndi vinyo ai;
22. atero Ambuye ako Yehova, ndi Mulungu wako amene anena mlandu wa anthu ace, Taona, ndacotsa m'dzanja mwako cikho conjenjemeretsa, ngakhale mbale ya cikho ca ukali wanga; iwe sudzamwa ico kawirinso.
23. Ndidzaciika m'dzanja la iwo amene abvutitsa iwe; amene anena ku moyo wako, Gwada pansi kuti ife tipite; ndipo iwe wagonetsa pamsana pako monga pansi, ndi monga khwalala kwa iwo amene apita pamenepo.