atero Ambuye ako Yehova, ndi Mulungu wako amene anena mlandu wa anthu ace, Taona, ndacotsa m'dzanja mwako cikho conjenjemeretsa, ngakhale mbale ya cikho ca ukali wanga; iwe sudzamwa ico kawirinso.