9. Akadapanda Yehova wa makamu kutisiyira otsala ang'onong'ono ndithu, ife tikanakhala ngati Sodomu, ife tikadanga Gomora.
10. Imvani mau a Yehova inu olamulira a Sodomu, cherani makutu ku cilamulo ca Mulungu wathu, inu anthu a Gomora.
11. Nditani nazo nsembe zanu zocurukazo? ati Yehova; ndakhuta nazo nsembe zopsereza za nkhosa zamphongo ndi mafuta a nyama zonenepa; sindisekera ndi mwazi wa ng'ombe zamphongo, ngakhale wa ana a nkhosa, ngakhale wa atonde.
12. Pakudzaonekera inu pamaso pa Ine, ndani wafuna cimeneci m'dzanja lanu, kupondaponda m'mabwalo mwanga?
13. Musadze nazonso, nsembe zacabecabe; nsembe zofukiza zindinyansa; tsiku lokhala mwezi ndi sabata, kumema masonkhano, sindingalole mphulupulu ndi masonkhano.