29. Ife tamva kudzikuza kwa Moabu, wadzikuza ndithu, kunyang'wa kwace, ndi kunyada kwace, ndi kudzitama kwace, ndi kudzikuza kwa mtima wace.
30. Ine ndidziwa mkwiyo wace, ati Yehova, kuti uli cabe; zonyenga zace sizinacita kanthu.
31. Cifukwa cace ndidzakuwira Moabu; inde, ndidzapfuulira Moabu yense, adzalirira anthu a ku Kirere.
32. Iwe mpesa wa Sibima; ndidzakulirira iwe ndi kulira kopambana kulira kwa Yazeri, nthambi zako zinapitirira nyanja, zinafikira ku nyanja ya Yazeri; wakufunkha wagwera zipatso zako za mpakasa ndi mphesa zako.
33. Ndipo kusekera ndi kukondwa kwacotsedwa, ku munda wobala ndi ku dziko la Moabu; ndipo ndaletsa vinyo pa zoponderamo; sadzaponda ndi kupfuula; kupfuula sikudzakhala kupfuula.
34. Kuyambira kupfuula kwa Hesiboni mpaka ku Eleale, mpaka ku Yahazi anakweza mau, kuyambira pa Zoari mpaka ku Horonaimu, ku Egilati-Selisiya; pakuti pa madzi a ku Nimurimu komwe padzakhala mabwinja.
35. Ndiponso ndidzaletsa m'Moabu, ati Yehova, iye amene apereka nsembe pamsanje, ndi iye amene afukizira milungu yace.