23. Koma Yehova Mulungu wanu adzawapereka pamaso panu, nadzawapitikitsa ndi kupitikitsa kwakukuru, kufikira ataonongeka.
24. Adzaperekanso mafumu ao m'dzanja mwanu, ndipo muwafafanize maina ao pansi pa thambo; palibe munthu mmodzi adzaima pamaso panu, kufikira mutawaononga,
25. Mafano osema a milungu yao muwateothe ndi moto; musamasirira siliva ndi golidi ziri pa iwo, kapena kudzitengera izi; mungakodwe nazo; pakuti izi zinyansira Yehova Mulungu wanu.
26. Musamalowa naco conyansaci m'nyumba mwanu, kuti mungaonongeke konse pamodzi naco; muziipidwa naco konse, ndi kunyansidwa naco konse; popeza ndi cinthu coyenera kuonongeka konse.