15. Pomwepo Isiboseti anatumiza namcotsera kwa mwamuna wace, kwa Palitieli mwana wa Laisi.
16. Ndipo mwamuna waceyo anapita naye, nanka nalira, namtsata kufikira ku Baburimu. Pomwepo Abineri ananena naye, Coka, bwerera; ndipo anabwerera.
17. Ndipo Abineri analankhula nao akuru a Israyeli nanena nao, Inu munayamba kale kufuna Davide akhale mfumu yanu;
18. citani tsono, popeza Yehova analankhula za Davide, kuti, a Ndi dzanja la Davide mnyamata wanga ndidzapulumutsa anthu anga Aisrayeli ku dzanja la Afilisti, ndi ku dzanja la adani ao onse.