Ndipo anyamata a Abisalomu anamcitira Amnoni monga umo Abisalomu anawalamulira. Pomwepo ana amuna onse a mfumu ananyamuka, nakwera munthu yense pa nyuru yace, nathawa.