6. Ndipo pamene ana a Amoni anazindikira kuti anadzinunkhitsa kwa Davide, ana a Amoniwo anatumiza nadzilembera Aaramu a ku Betirehobu, ndi Aaramu a ku Zoba, oyenda pansi zikwi makumi awiri, ndi mfumu ya ku Maaka ndi anthu cikwi cimodzi, ndi anthu a mfumu ya ku Tobu zikwi khumi ndi ziwiri.
7. Ndipo pamene Davide anacimva, anatumiza Yoabu ndi khamu lonse la anthu amphamvu.
8. Ndipo ana a Amoni anaturuka, nandandalitsa nkhondo polowera kucipata. Ndipo Aaramu a ku Zoba ndi a ku Rehobu, ndi anthu a Tobu ndi Maaka, anali pa okha kuthengo.
9. Ndipo pamene Yoabu anaona kuti nkhondo inamdzera kumaso ndi kumbuyo, iye anasankha amuna osankhidwa onse a Israyeli, nawandandalitsa ca kwa Aramu.
10. Koma anthu otsalawo anawapereka kwa Abisai mbale wace, amene anawandandalitsa ca kwa Amoni.
11. Ndipo iye anati, Aaramu akandipambana ine, udzandithandiza ndiwe, koma ana a Amoni akapambana iwe, tsono ndidzabwera ine kukuthandiza.
12. Ulimbike mtima, ndipo ticite camuna lero cifukwa ca anthu athu ndi midzi ya Mulungu wathu; Yehova nacite comkomera.
13. Comweco Yoabu ndi anthu amene anali naye anayandikira kuponyana nkhondo ndi Aaramu. Ndipo iwowa anathawa pamaso pace.