7. Yehova asaukitsa, nalemeza;Acepetsa, nakuzanso.
8. Amuutsa waumphawi m'pfumbi,Nanyamula wosowa padzala,Kukamkhalitsa kwa akalonga;Ndi kuti akhale naco colowa ca cimpando ca ulemerero;Cifukwa nsanamira za dziko lapansi nza Yehova,Ndipo iye anakhazika dziko pa izo,
9. Adzasunga mapazi a okoodedwaace,Koma oipawo adzawakhalitsa cete mumdima;Pakuti palibe munthu adzapambana ndi mphamvu,
10. Otsutsana ndi Yehova adzaphwanyika;Kumwamba iye adzagunda pa iwo:Yehova adzaweruza malekezero a dziko:Ndipo adzapatsa mphamvu mfumuyace,Nadzakweza nyanga ya wodzozedwa wace.
11. Ndipo Elikana anauka kwao ku Rama, mwanayo natumikira Yehova pamaso pa Eli wansembeyo.
12. Koma ana a Eli anali oipa; sanadziwa Yehova.
13. Ndipo macitidwe a ansembe akucitira anthu ndiwo, kuti pamene munthu ali yense akapereka nsembe, mnyamata wa wansembeyo akabwera, nyama iri ciwirire, ndi cobvuulira ca ngowe ca mana atatu m'dzanja lace;
14. nacipisa m'cimphuli, kapena mumkhate, kapena m'nkhali, kapena mumphika; yonse imene cobvuuliraco cinaiturutsa, wansembeyo anaitenga ikhale yace. Adafotero ku Silo ndi Aisrayeli onse akufika kumeneko.