Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yuda 1:10-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Koma iwowa zimene sazidziwa azicitira mwano; ndipo zimene azizindikira cibadwire, monga zamoyo zopanda nzeru, mu izi atayika,

11. Tsoka kwa iwo! pakuti anayenda m'njira ya Kaini, ndipo anadziononga m'cisokero ca Balamu cifukwa ca kulipira, natayika m'citsutsano ca Kore,

12. Iwo ndiwo okhala mawanga pa mapwando anu a cikondano, pakudya nanu pamodzi, akudziweta okha opanda mantha; mitambo yopanda madzi, yotengekatengeka ndi mphepo; mitengo ya masika yopanda zipatso, yofafa kawid, yozuka mizu;

13. mafunde oopsya a nyanja, akuwinduka thobvu la manyazi a iwo okha; nyenyezi zosokera, zimene mdima wakuda bii udazisungikira kosatha.

14. Ndipo kwa iwo, Henoke, wacisanu ndi ciwiri kuyambira kwa Adamu, ananenera kuti, Taona, wadza Ambuye ndi oyera ace zikwi makumi,

15. kudzacitira onse ciweruziro, ndi kutsutsa osapembedza onse, pa nchito zao zonse zosapembedza, zimene anazicita kosapembedza, ndi pa zolimba zimene ocimwa osapembedza adalankhula pa iye.

16. Amenewo ndiwo odandaula, oderera, akuyenda monga mwa zilakolako zao (ndipo pakamwa pao alankhula zazikuruzikuru), akutama anthu cifukwa ca kupindula nako.

17. Koma inu, abale, mukumbukile mau onenedwa kale ndi atumwi a Ambuye wathu Yesu Kristu;

18. kuti ananena nanu, 1 Pa nthawi yotsiriza padzakhala otonza, akuyenda monga mwa zilakolako zosapembedza za iwo okha.

19. Iwo ndiwo opatukitsa, anthu a makhalidwe acibadwidwe, osakhala naye Mzimu.

20. Koma inu, okondedwa, 3 podzimangirira nokha pa cikhulupiriro canu coyeretsetsa, ndi 4 kupemphera mu Mzimu Woyera,

Werengani mutu wathunthu Yuda 1