Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 6:23-40 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

23. koma zinacokera ngalawa zina ku Tiberiya, pafupi pa malo pomwe adadyapo mkate m'mene Yesu adayamika;

24. cifukwa cace pamene khamu la anthu linaona kuti palibe Yesu, ndi akuphunzira ace palibe, iwo okha analowa m'ngalawazo nadza ku Kapernao, alikufuna Yesu.

25. Ndipo pamene anampeza iye tsidya lina la nyanja, anati kwa iye, Rabi, munadza kuno liti?

26. Yesu anayankha iwo nati, Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Mundifuna Ine, si cifukwa munaona zizindikilo, koma cifukwa munadya mkate, nimunakhuta.

27. Gwirani nchito si cifukwa ca cakudya cimene citayika koma ca cakudya cimene citsalira ku moyo wosatha, cimene Mwana wa munthu adzakupatsani inu; pakuti ameneyo Atate, ndiye Mulungu, adamlembera cizindikilo.

28. Pamenepo anati kwa iye, Ticite ciani, kuti ticite nchito za Mulungu?

29. Yesu anayankha nati kwa iwo, Nchito ya Mulungu ndi iyi, kuti mukhulupirire iye amene Iyeyo anamtuma.

30. Cifukwa cace anati kwa iye, Ndipo mucita cizindikilo canji, kuti tione ndi kukhulupirira Inu? mucita ciani?

31. Atate athu anadya mana m'cipululu; monga kwalembedwa, Mkate wocokera m'mwamba anawapatsa iwo kudya,

32. Cifukwa cace Yesu anati kwa iwo, Indetu, indetu, ndinena kwa inu, Si Mose amene anakupatsani inu mkate wa Kumwamba; koma Atate wanga akupatsani inu mkate woona wa Kumwamba.

33. Pakuti mkate wa Mulungu ndiye wakutsika kucokera Kumwamba ndi kupatsa moyo kwa dziko lapansi.

34. Pamenepo anati kwa iye, Ambuye, tipatseni ife mkate umene nthawi zonse.

35. Yesu anati kwa iwo, Ine ndine mkate wamoyo; iye amene adza kwa Ine sadzamva njala, ndi iye amene akhulupirira Ine sadzamva ludzu nthawi zonse.

36. Koma ndinati kwa inu, kuti mungakhale mwandiona, simukhulupirira.

37. Cinthu conse cimene anandipatsa Ine Atate cidzadza kwa Ine; ndipo wakudza kwa Ine sindidzamtaya iye kunja.

38. Pakuti ndinatsika Kumwamba, si kuti ndicite cifuniro canga, koma cifuniro ca iye amene anandituma Ine.

39. Koma cifuniro ca Iye amene anandituma Ine ndi ici, kuti za ici conse Iye anandipatsa Ine ndisatayeko kanthu, koma ndiciukitse tsiku lomariza.

40. Pakuti cifuniro ca Atate wanga ndi ici, kuti yense wakuyang'ana Mwana, ndi kukhulupirira iye, akhale nao moyo wosatha; ndipo Ine ndidzamuukitsa iye tsiku lomariza.

Werengani mutu wathunthu Yohane 6