Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 5:19-38 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Pamenepo Yesu anayankha nati kwa iwo, Indetu, indetu, ndinena kwa inu, sakhoza Mwana kucita kanthu pa yekha, koma cimene aona Atate acicita, ndico. Pakuti zimene iye azicita, zomwezo Mwananso azicita momwemo.

20. Pakuti Atate akonda Mwana, namuonetsa zonse azicita yekha: ndipo adzamuonetsa nchito zoposa izi, kuti mukazizwe,

21. Pakuti monga Atate aukitsa akufa, nawapatsa moyo, momwemonso Mwanaapatsa moyo iwo amene iye afuna.

22. Pakuti Atate saweruza munthu ali yense, koma anapereka kuweruza konse kwa Mwana;

23. kuti onse akalemekeze Mwana, monga alemekeza Atate. Wosalemekeza Mwana salemekeza Atate amene anamtuma iye.

24. Indetu, indetu, ndinena kwa inu, kuti iye wakumva mau anga, ndi kukhulupirira iye amene anandituma Ine, ali nao moyo wosatha, ndipo salowa m'kuweruza, koma wacokera kuimfa, nalowa m'moyo.

25. Indetu, indetu, ndinena kwa inu, kuti ikudza nthawi, ndipo Iripo tsopano, imene akufa adzamva mau a Mulungu; ndipo iwo akumva adzakhala ndi moyo.

26. Pakuti monga Atate ali ndi moyo mwa iye yekha, momwemonso anapatsa kwa Mwana kukhala ndi moyo mwa iye yekha;

27. ndipo anampatsa iye mphamvu ya kucita mlandu, pakuti ali Mwana wa munthu.

28. Musazizwe ndi ici, kuti ikudza nthawi, imene onse ali m'manda adzamva mau ace,

29. nadzaturukira, amene adacita zabwino, kukuuka kwa moyo; koma amene adacita zoipa kukuuka kwa kuweruza.

30. Sindikhoza kucita kanthu kwa Ine ndekha; monga momwe ndimva ndiweruza; ndipo maweruzidwe anga ali olungama; cifukwa kuti sinditsata cifuniro canga, koma cifuniro ca Iye ondituma Ine.

31. Ngati ndicita umboni wa Ine ndekha, umboni wanga suli woona.

32. Wocita umboni wa Ine ndi wina; ndipo ndidziwa kuti umboni umene iye andicitira Ine uli woona.

33. Inu munatuma kwa Yohane, ndipo iye anacitira umboni coonadi.

34. Ndipo Ine sindilandira umboni kwa munthu: koma ndinena izi, kuti inu mukapulumutsidwe.

35. Iyeyo anali nyali yoyaka ndi yowala; ndipo inu munafuna kukondwera m'kuunika kwace kanthawi.

36. Koma Ine ndiri nao umboni woposa wa Yohane; pakuti nchito zimene Atateanandipatsa ndizitsirize, nchito zomwezo ndizicita zindicitira umboni, kuti Atate anandituma Ine.

37. Ndipo Atate wonditumayo, 1 Iyeyu wandicitira Ine umboni. Simunamva mau ace konse, kapena maonekedwe ace simunaona.

38. Ndipo mulibe mau ace okhala mwa inu; cifukwa kuti amene Iyeyu anatuma, inu simumkhulupirira ameneyo.

Werengani mutu wathunthu Yohane 5