Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 21:15-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Ndipo pamene atafisula Yesu ananena kwa Simoni Petro, Simoni mwana wa Yona, kodi undikonda Ine koposa awa? Ananena ndi iye, Inde, Ambuye; mudziwa kuti ndikukondani Inu. Ananena naye, Dyetsa ana a nkhosa anga.

16. Ananena nayenso kaciwiri, Simoni mwana wa Yona, ukonda Ine kodi? Ananena ndi iye, Inde, Ambuye; mudziwa kuti ndikukondani Inu. Ananena naye, Weta nkhosa zanga.

17. Ananena: naye kacitatu, Simoni mwana wa Yona, kodi undikonda Ine? Petro anamva cisoni kuti anati kwa iye kacitatu, Kodi undikonda Ine? ndipo anati kwa iye, Ambuye, mudziwa Inu zonse; muzindikira kuti ndikukondani Inu. Yesu ananena naye, Dyetsa nkhosa zanga.

18. Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, pamene unali mnyamata unadzimangira wekha m'cuuno, ndipo unayenda kumene unafuna; koma pamene udzakalamba udzaturutsa manja ako, ndipo adzakumanga wina, nadzakunyamula kumene sufuna.

19. Koma ici ananena ndi kuzindikiritsa imfa imene adzalemekeza nayo Mulungu. Ndipo m'mene ananena ici, anati kwa iye, nditsate Ine,

Werengani mutu wathunthu Yohane 21