Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 20:14-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. M'mene adanena izi, anaceuka m'mbuy'o, naona Yesu ali ciriri, ndipo sanadziwa kuti ndiye Yesu.

15. Yesu ananena naye, Mkazi, uliranji? ufuna yani? Iyeyu poyesa kuti ndiye wakumunda, ananena ndi iye, Mbuye ngati mwamnyamula iye, ndiuzeni kumene mwamuika iye, ndipo ndidzamcotsa.

16. Yesu ananena naye, Mariya. Iyeyu m'mene anaceuka, ananena ndi iye m'Cihebri, Raboni; cimene cinenedwa, Mphunzitsi.

17. Yesu ananena naye, Usandikhudze, pakuti sindinatha kukwera kwa Atate; koma pita kwa abale anga, ukati kwa iwo, Ndikwera kunka kwa Atate wanga, ndi Atate wanu, ndi Mulungu wanga, ndi Mulungu wanu.

18. Mariya wa Magadala anapita nalalikira kwa akuphunzirawo, kuti, Ndaona Ambuye; ndi kuti ananena izi kwa iye.

19. Pamenepo, pokhala madzulo, tsiku lomwelo, loyamba la Sabata, makomo ali citsekere, kumene anakhala akuphunzira, cifukwa ca kuopa Ayuda, Yesu anadza naimirira pakati pao, nanena nao, Mtendere ukhale ndi inu.

20. Ndipo pamene adanena ici, anaonetsa iwo manja ace ndi nthiti zace. Pamenepo akuphunzira anakondwera pakuona Ambuye.

21. Cifukwa cace Yesu anatinso kwa iwo, Mtendere ukhale ndi inu; monga Atate wandituma Ine, Inenso ndituma inu.

22. Ndipo pamene anati ici anawapumira, nanena nao, Landirani Mzimu Woyera.

23. Zocimwa za anthu ali onse muwakhululukira, zikhululukidwa kwa iwo; za iwo amene muzigwiritsa, zagwiritsidwa.

24. Koma Tomasi, mmodzi wa khumi ndi awiriwo, wochedwa Didimo, sanakhala nao pamodzi, pamene Yesu anadza.

25. Cifukwa cace akuphunzira ena ananena naye, Tamuona Ambuye. Koma iye anati kwa iwo, Ndikapanda kuona m'manja ace cizindikilo ca misomaliyo, ndi kuika cala canga m'cizindikilo ca misomaliyo, ndi kuika dzanja langa ku nthiti yace; sindidzakhulupira.

26. Ndipo pakupita masiku asanu ndi atatu akuphunzira ace analinso m'nyumbamo, ndi Tomasi pamodzi nao: Yesu anadza, makomo ali citsekere, naimirira pakati, nati, Mtendere ukhale ndi inu.

27. Pomwepo ananena kwa Tomasi, Bwera naco cala cako kuno, nuone manja anga; ndipo bwera nalo dzanja lako, nuliike ku nthiti yanga, ndipo usakhale wosakhulupira, koma wokhulupira.

Werengani mutu wathunthu Yohane 20