Cifukwa cace akuphunzira ena ananena naye, Tamuona Ambuye. Koma iye anati kwa iwo, Ndikapanda kuona m'manja ace cizindikilo ca misomaliyo, ndi kuika cala canga m'cizindikilo ca misomaliyo, ndi kuika dzanja langa ku nthiti yace; sindidzakhulupira.