Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 15:9-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Monga momwe Atate wandikonda Ine, Inenso ndakonda inu; khalani m'cikondi canga.

10. Ngati musunga malamulo anga mudzakhala m'cikondi canga; monga Ine ndasunga malamulo a Atate wanga, ndipo ndikhala m'cikondi cace.

11. Izi ndalankhula ndi inu, kuti cimwemwe canga cikhale mwa inu, ndi kuti cimwemwe canu cidzale.

12. Lamulo langa ndi ili, kuti mukondane wina ndi mnzace, monga ndakonda inu.

13. Palibe munthu ali naco cikondi coposa ici, cakuti munthu ataya moyo wace cifukwa ca abwenzi ace.

14. Muli abwenzianga inu, ngati muzicita zimene ndikulamulirani inu.

15. Sindichanso inu akapolo; cifukwa kapolo sadziwa cimene mbuye wace acita; koma ndacha inu abwenzi; cifukwa zonse zimene ndazimva kwa Atate wanga ndakudziwitsani.

16. Inu simunandisankha Ine, koma Ine ndinakusankhani inu, ndipo ndinakuikani, kuti mukamuke inu ndi kubala cipatso, ndi kuti cipatso canu cikhale; kuti cimene ciri conse mukapempha Atate m'dzina langa akakupatseni inu.

17. Zinthu izi ndilamulira inu, kuti mukondane wina ndi mnzace.

18. Ngati dziko lapansi lida inu, mudziwa kuti lidada Ine lisanayambe kuda inu.

19. Mukadakhala a dziko lapansi, dziko lapansi likadakonda zace za lokha; koma popeza simuli a dziko lapansi, koma Ine ndinakusankhani inu mwa dziko lapansi, cifukwa ca ici likudani inu.

20. Kumbukilani mau amene Ine ndinanena kwa inu, Kapolo sali wamkuru ndi mbuye wace. Ngati anandilondalonda Ine, adzakulonda-londani inunso; ngati anasunga mau anga, adzasunga anunso.

21. Koma izi zonse adzakucitirani cifukwa ca dzina langa, cifukwa sadziwa wondituma Ine.

22. Sindikadadza ndi kulankhula nao sakadakhala nalo cimo; koma tsopano alibe cowiringula pa macimo ao.

23. Iye wondida Ine, adanso Atate wanga.

24. Sindikadacita mwa iwo nchito zosacita wina, sakadakhala nalo cimo; koma tsopano anaona, nada: Ine ndi Atate wanganso,

25. Koma citero, kuti mau olembedwa m'cilamulo cao akwaniridwe, kuti, Anandida Ine kopanda cifukwa.

Werengani mutu wathunthu Yohane 15