Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 15:16-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Inu simunandisankha Ine, koma Ine ndinakusankhani inu, ndipo ndinakuikani, kuti mukamuke inu ndi kubala cipatso, ndi kuti cipatso canu cikhale; kuti cimene ciri conse mukapempha Atate m'dzina langa akakupatseni inu.

17. Zinthu izi ndilamulira inu, kuti mukondane wina ndi mnzace.

18. Ngati dziko lapansi lida inu, mudziwa kuti lidada Ine lisanayambe kuda inu.

19. Mukadakhala a dziko lapansi, dziko lapansi likadakonda zace za lokha; koma popeza simuli a dziko lapansi, koma Ine ndinakusankhani inu mwa dziko lapansi, cifukwa ca ici likudani inu.

20. Kumbukilani mau amene Ine ndinanena kwa inu, Kapolo sali wamkuru ndi mbuye wace. Ngati anandilondalonda Ine, adzakulonda-londani inunso; ngati anasunga mau anga, adzasunga anunso.

21. Koma izi zonse adzakucitirani cifukwa ca dzina langa, cifukwa sadziwa wondituma Ine.

22. Sindikadadza ndi kulankhula nao sakadakhala nalo cimo; koma tsopano alibe cowiringula pa macimo ao.

23. Iye wondida Ine, adanso Atate wanga.

24. Sindikadacita mwa iwo nchito zosacita wina, sakadakhala nalo cimo; koma tsopano anaona, nada: Ine ndi Atate wanganso,

25. Koma citero, kuti mau olembedwa m'cilamulo cao akwaniridwe, kuti, Anandida Ine kopanda cifukwa.

26. Koma pamene wafika Nkhoswe, amene Ine ndidzamtuma kwa inu kucokera kwa Atate, ndiye Mzimu wa coonadi, amene aturuka kwa Atate, Iyeyu adzandicitira Ine umboni.

27. Ndipo inunso mucita umboni, pakuti muli ndi Ine kuyambira ciyambi.

Werengani mutu wathunthu Yohane 15