Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 12:33-50 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

33. Koma ananena ici ndi kuzindikiritsa imfa yanji akuti adzafa nayo.

34. Pamenepo khamulo linayankha iye, Tidamva ife m'cilamulo kuti Kristu akhala ku nthawi yonse; ndipo Inu munena bwanji, kuti Mwana wa munthu ayenera kukwezedwa? Mwana wa munthu amene ndani?

35. Pamenepo Yesu anati kwa iwo, Katsala kanthawi kakang'ono ndipo kuunika kuli mwa inu. 1 Yendani pokhala muli nako kuunika, kuti mdima sungakupezeni; ndipo woyenda mumdima sadziwa kumene amukako,

36. 2 Pokhala muli nako kuunika, khulupirirani kuunikako, kuti mukakhale ana a kuunikako.Izi Yesu analankhula, nacoka nawabisalira.

37. Koma angakhale adacita zizindikilo zambiri zotere pamaso pao iwo sanakhulupirira iye;

38. kuti mau a Yesaya mneneri akakwaniridwe, amene anati,3 Ambuye, wakhulupirira ndani kulalikira kwathu?Ndipo mkono wa Ambuye wabvumbulutsidwa kwa yani?

39. Cifukwa ca ici sanathe kukhulupira, pakuti Yesaya anatinso,

40. 4 Wadetsa maso ao, naumitsa mtima wao;Kuti angaone ndi maso, angazindikire ndi mtima,Nangatembenuke,Ndipo ndingawaciritse.

41. 5 Izi anati Yesaya, cifukwa anaona ulemerero wace; nalankhula za iye.

42. Kungakhale kotero, ambiri a mwa akuru anakhulupirira iye; koma 6 cifukwa ca Afarisi sanabvomereza, kuti angaletsedwe m'sunagoge,

43. 7 pakuti anakonda ulemerero wa anthu koposa ulemerero wa Mulungu.

44. Koma Yesu anapfuula nati, 8 iye wokhulupirira ine, sakhulupirira Ine, koma iye wondituma Ine.

45. Ndipo 9 wondiona Ine aona amene anandituma Ine

46. 10 Ndadza Ine kuunika ku dziko lapansi, kuti yense wokhulupirira Ine asakhale mumdima.

47. Ndipo ngati wina akumva mau anga, ndi kusawasunga, Ine sindimweruza; pakuti 11 sindinadza kudzaweruza dziko lapansi, koma kuti ndipulumutse dziko lapansi.

48. 12 iye amene akaniza Ine, ndi kusalandira mau anga, ali naye womweruza iye; 13 mau amene ndalankhula, iwowa adzamweruza tsiku lomariza.

49. 14 Pakuti sindinalankhula mwa Ine ndekha; koma Atate wondituma Ine, yemweyu anandipatsa Ine lamulo, limene ndikanene, ndi limene ndikalankhule.

50. Ndipo ndidziwa kuti lamulo lace liri moyo wosatha; cifukwa cace zimene ndilankhula, monga momwe Atate wanena ndi Ine, momwemo ndilankhula.

Werengani mutu wathunthu Yohane 12