Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Marko 9:22-35 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

22. Ndipo kawiri kawiri ukamtaya kumoto ndi kumadzi, kumuononga; koma ngati mukhoza kucita kanthu mtithandize, ndi kuticitira cifundo.

23. Ndipo Yesu ananena naye, Ngati mukhoza! Zinthu zonse zitheka ndi iye wakukhulupirira.

24. Pomwepo atate wa mwana anapfuula, nanena, Ndikhulupirira; thandizani kusakhulupirira kwanga.

25. Ndipo pamene Yesu anaona kuti khamu la anthu lirikuthamangira pamodzi, anadzudzula mzimu woipawo, nanena ndi uwo, Mzimu wosalankhula ndi wogontha iwe, Ine ndikulamula iwe, turuka mwa iye, ndipo usalowenso mwa iye.

26. Ndipo pamene unapfuula, numng'ambitsa, unaturuka; ndipo mwana anakhala ngati wakufa; kotero kuti ambiri ananena, Wamwalira.

27. Koma Yesu anamgwira dzanja lace, namnyamutsa; ndipo anaimirira.

28. Ndipo pamene Iye adalowa m'nyumba, ophunzira ace anamfunsa m'tseri, kuti, Nanga bwanji sitinakhoza ife kuuturutsa?

29. Ndipo Iye anati kwa iwo, Mtundu uwu sukhoza kuturuka ndi kanthu kena konse, koma ndi kupemphera.

30. Ndipo anacoka iwo kumeneko, napyola pakati pa Galileya; ndipo Iye sanafuna kuti munthu adziwe.

31. Pakuti anaphunzitsa ophunzira ace, nanena nao, kuti, Mwana wa munthu aperekedwa m'manja a anthu, ndipo adzamupha Iye; ndipo ataphedwa, adzauka pofika masiku atatu.

32. Koma iwo sanazindikira mauwo, naopa kumfunsa.

33. Ndipo iwo anadza ku Kapernao; ndipo pamene anakhala m'nyumba, Iye anawafunsa, Munalikutsutsana ninji panjira?

34. Koma iwo anakhala cete; pakuti anatsutsana wina ndi mnzace panjira, kuti, wamkuru ndani?

35. Ndipo m'mene anakhala pansi anaitana khumi ndi awiriwo; nanena nao, Ngati munthu afuna kukhala woyamba, akhale wakuthungo wa onse, ndi mtumiki wa onse.

Werengani mutu wathunthu Marko 9