Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Marko 6:4-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Ndipo Yesu ananena kwa iwo, Mneneri sakhala wopanda ulemu, koma m'dziko la kwao ndimo, ndi pakati pa abale ace, ndi m'nyumba yace.

5. Ndipo kumeneko sanakhoza Iye kucita zamphamvu konse, koma kuti anaika manja ace pa anthu odwala owerengeka, nawaciritsa.

6. Ndipo anazizwa cifukwa ca kusakhulupirira kwao. Ndipo anayendayenda m'midzi yozungulirapo, naphunzitsa.

7. Ndipo anadziitanira khumi ndi awiriwo, nayamba kuwatumiza Iwo awiri awiri; nawapatsa mphamvu pa mizimu yonyansa;

8. ndipo anawauza kuti asatenge kanthu ka paulendo, koma ndodo yokha; asatenge mkate, kapena thumba, kapena ndalama m'lamba lao;

9. koma abvale nsapato; ndipo anati, Musabvale malaya awiri.

10. Ndipo ananena nao, Kumene kuli konse mukalowa m'nyumba, khalani komweko kufikira mukacokako.

11. Ndipo pamalo ponse sakulandirani, kapena kumvera inu, pakucoka kumeneko, sansani pfumbi liri ku mapazi anu, likhale mboni ya kwa iwo.

12. Ndipo anaturuka nalalikira kuti anthu atembenuke mitima.

13. Ndipo anaturutsa mizimu yoipa yambiri, nadzoza mafuta anthu ambiri akudwala, nawaciritsa.

14. Ndipo mfumu Herode anamva izi; pakuti dzina lace lidamveka; ndipo ananena, kuti, Yohane Mbatizi wauka kwa akufa, ndipo cifukwa cace mphamvu izi zicitacita mwa Iye.

15. Koma ena ananena, kuti, Ndiye Eliya, Anati enanso, Ndiye mneneri, monga ngati mmodzi wa aneneriwo,

Werengani mutu wathunthu Marko 6