Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Marko 6:2-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Ndipo pofika dzuwa la Sabata, anayamba kuphunzitsa m'sunagoge; ndipo ambiri anamva Iye, nazizwa, nanena, Uyu adazitenga kuti izi? Nzeru yopatsidwa kwa munthuyu njotani, ndi zamphamvu zotere zocitidwa ndi manja ace?

3. Si mmisiri wa mitengo uyu, mwana wa Mariya, mbale wao wa Yakobo, ndi Yose, ndi Yuda, ndi Simoni? Ndipo alongo ace sali nafe pano kodi? Ndipo anakhumudwa ndi Iye.

4. Ndipo Yesu ananena kwa iwo, Mneneri sakhala wopanda ulemu, koma m'dziko la kwao ndimo, ndi pakati pa abale ace, ndi m'nyumba yace.

5. Ndipo kumeneko sanakhoza Iye kucita zamphamvu konse, koma kuti anaika manja ace pa anthu odwala owerengeka, nawaciritsa.

Werengani mutu wathunthu Marko 6