Ndipo pofika dzuwa la Sabata, anayamba kuphunzitsa m'sunagoge; ndipo ambiri anamva Iye, nazizwa, nanena, Uyu adazitenga kuti izi? Nzeru yopatsidwa kwa munthuyu njotani, ndi zamphamvu zotere zocitidwa ndi manja ace?