Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Marko 6:13-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Ndipo anaturutsa mizimu yoipa yambiri, nadzoza mafuta anthu ambiri akudwala, nawaciritsa.

14. Ndipo mfumu Herode anamva izi; pakuti dzina lace lidamveka; ndipo ananena, kuti, Yohane Mbatizi wauka kwa akufa, ndipo cifukwa cace mphamvu izi zicitacita mwa Iye.

15. Koma ena ananena, kuti, Ndiye Eliya, Anati enanso, Ndiye mneneri, monga ngati mmodzi wa aneneriwo,

16. Koma Herode pamene anamva, ananena, Yohane amene ndamdula mutu, wauka iyeyo.

17. Pakuti Herode, mwini yekha, adatuma anthu namgwira Yohane, nammanga m'nyumba yandende, cifukwa ca Herodiya, mkazi wa Filipo mbale wace; cifukwa adamkwatira iye.

18. Pakuti Yohane adanena kwa Herode, Si kuloledwa kwa inu kukhala naye mkazi wa mbale wanu.

19. Ndipo Herodiya anamuda, nafuna kumupha; koma sanakhoza;

20. pakuti Herode anaopa Yohane, podziwa kuti ali munthu wolungama ndi woyera mtima, ndipo anamsunga iye. Ndipo pamene anamva iye anathedwa nzeru, oakondwa kumva iye.

21. Ndipo pamene panafika tsiku loyenera, tsiku la kubadwa kwace kwa Herode, iye anawakonzera phwando akuru ace ndi akazembe ace ndi anthu omveka a ku Galileya;

22. ndipo pamene mwana wamkazi wa Herodiya analowa yekha nabvina, anakondwetsa Herode ndi iwo akukhala naye pacakudya; ndipo mfumuyo inati kwa buthulo, Tapempha kwa ine ciri conse ucifuna, ndidzakupatsa iwe.

23. Ndipo anamlumbirira iye, kuti, Ciri conse ukandipempha ndidzakupatsa, kungakhale kukugawira ufumu wanga.

24. Ndipo anaturuka, nati kwa amace, Ndidzapempha ciani? Ndipo iyel anati, Mutu wace wa Yohane Mbatizi.

25. Ndipo pomwepo analowa m'mangu m'mangu kwa mfumu, napempha kuti, Ndifuna kuti mundipatse tsopano apa, mutu wace wa Yohane Mbatizi mumbizi.

Werengani mutu wathunthu Marko 6