Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Marko 2:8-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Ndipo pomwepo Yesu pozindikira mumtima mwace kuti alikuganizira comweco mwa iwo okha, ananena nao, Muganiza bwanji zinthu izi m'mitima yanu?

9. Capafupi nciti, kapena kuuza wodwala manjenje kuti, Macimo ako akhululukidwa; kapena kuti, Nyamuka, senza mphasa yako, nuyende?

10. Koma kuti mudziwe kuti Mwana wa munthu ali mwini ulamuliro wakukhululukira macimo pa dziko lapansi (ananena ndi wodwala manjenje),

11. Ndikuuza iwe, Nyamuka, senza mphasa yako, numuke kwanu.

12. Ndipo ananyamuka iye pomwepo, nasenza mphasa, naturuka pamaso pa iwo onse; kotero kuti anadabwa onse, nalemekeza Mulungu, nanena kuti, Zotere sitinaziona ndi kale lonse.

13. Ndipo anaturukanso kunka m'mbali mwa nyanja; ndipo linadza kwa Iye khamu lonse la anthu, ndipo anawaphunzitsa.

Werengani mutu wathunthu Marko 2