Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Marko 2:10-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Koma kuti mudziwe kuti Mwana wa munthu ali mwini ulamuliro wakukhululukira macimo pa dziko lapansi (ananena ndi wodwala manjenje),

11. Ndikuuza iwe, Nyamuka, senza mphasa yako, numuke kwanu.

12. Ndipo ananyamuka iye pomwepo, nasenza mphasa, naturuka pamaso pa iwo onse; kotero kuti anadabwa onse, nalemekeza Mulungu, nanena kuti, Zotere sitinaziona ndi kale lonse.

13. Ndipo anaturukanso kunka m'mbali mwa nyanja; ndipo linadza kwa Iye khamu lonse la anthu, ndipo anawaphunzitsa.

14. Ndipo pakumuka, anaona Levi mwana wa Alifeyu alikukhala polandira msonkho, ndipo ananena naye, Tsata Ine.

15. Ndipo ananyamuka namtsata Iye. Ndipo kunali kuti anakhala pakudya m'nyumba mwace, ndipo amisonkho ndi ocimwa ambiri anakhala pansi pamodzi ndi Yesu ndi ophunzira ace, pakuti anali ambiri, ndipo anamtsata Iye.

16. Ndipo alembi a kwa Afarisi, pakuona kuti alinkudya nao ocimwa ndi amisonkho, ananena ndi ophunzira ace, Uyu akudya ndi kumwa nao amisonkho ndi ocimwa.

17. Ndipo pamene Yesu anamva ici, ananena nao, Akulimba safuna sing'anga, koma odwala ndiwo; sindinadza kudzaitana olungama, koma ocimwa.

18. Ndipo ophunzira a Yohane ndi Afarisi analinkusala kudya; ndipo anadza, nanena ndi Iye, Bwanji asala kudya ophunzira a Yohane, ndi ophunzira a Afarisi, koma ophunzira anu sasala kudya?

Werengani mutu wathunthu Marko 2