Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Marko 16:6-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Ndipo iye ananena nao, Musadabwe: mulikufuna Yesu Mnazarene amene anapacikidwa: anauka; sali pano; taonani, mbuto m'men e anaikamo Iye!

7. Koma mukani, uzani ophunzira ace, ndi Petro, kuti akutsogolerani inu ku Galileya; kumeneko mudzamuona Iye, monga ananena ndi inu.

8. Ndipo anaturuka iwo, nathawa kumanda; pakuti kunthunthumira ndi kudabwa kwakukuru kudawagwira; ndipo sanauza kanthu kwa munthu ali yense; pakuti anacitamantha.

9. Ndipo pamene Iye adauka mamawa tsiku loyamba la sabata, anayamba kuonekera kwa Maliya wa Magadala, amene Iye adamturutsira ziwanda zisanu ndi ziwiri.

10. Iyeyu anapita kuwauza iwo amene adafokhala naye, ali ndi cisoni ndi kulira misozi.

11. Ndipo iwowo, pamene anamva kuti ali moyo, ndi kuti adapenyeka kwa iye, sanamvera.

12. Ndipo zitatha izi, anaonekanso Iye m'maonekedwe ena kwa awiri a iwo alikuyenda kupita kumiraga,

13. Ndipo iwowa anacoka nawauza otsala; koma iwo omwe sanawabvomereza.

14. Ndipo citatha ico anaonekera kwa khumi ndi mmodzi iwo okha, alikuseama pacakudya; ndipo anawadzudzula cifukwa ca kusabvomereza kwao ndi kuuma mtima, popeza sanabvomereza iwo amene adamuona, atauka Iye.

15. Ndipo ananena nao, mukani ku dziko lonse lapansi, lalikirani Uthenga Wabwino kwa olengedwa onse.

16. Amene akhulupirira nabatizidwa, adzapulumutsidwa; koma amene sakhulupirira adzalangidwa.

Werengani mutu wathunthu Marko 16