Ndipo citatha ico anaonekera kwa khumi ndi mmodzi iwo okha, alikuseama pacakudya; ndipo anawadzudzula cifukwa ca kusabvomereza kwao ndi kuuma mtima, popeza sanabvomereza iwo amene adamuona, atauka Iye.