Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Marko 10:32-49 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

32. Ndipo iwo anali m'njira alinkukwera kunka ku Yerusalemu; ndipo Yesu analikuwatsogolera; ndipo iwo anazizwa; ndipo akumtsatawo anacita mantha. Ndipo Iye anatenganso khumi ndi awiriwo, nayamba kuwauza zinthu zimene zidzamfikira Iye,

33. nati, Taonani, tikwera ku Yerusalemu; ndipo Mwana wa munthu adzaperekedwa kwa ansembe akuru ndi alembi; ndipo iwo adzamweruza kuti ayenera imfa, nadzampereka Iye kwa anthu a mitundu;

34. ndipo adzamnyoza Iye, nadzamthira malobvu, nadzamkwapula Iye, nadzamupha; ndipo pofika masiku atatu adzauka.

35. Ndipo anadza kwa Iye Yakobo ndi Yohane, ana a Zebedayo, nanena naye, Mphunzitsi, tifuna kuti mudzaticitire cimene ciri conse tidzapempha kwa Inu.

36. Ndipo Iye anati kwa iwo, Mufuna kuti ndidzakucitireni inu ciani?

37. Ndipo iwo anati kwa Iye, Mutipatse ife kuti tikhale mmodzi ku dzanja lanu lamanja, ndi wina kulamanzere, m'ulemerero wanu.

38. Koma Yesu anati kwa iwo, Simudziwa cimene mucipempha, Mukhoza kodi kumwera cikho cimene ndimwera Ine? kapena kubatizidwa ndi ubatizo umene ndibatizidwa nao Ine?

39. Ndipo anati kwa Iye, Tikhoza. Ndipo Yesu anati kwa iwo, Cikho cimene ndimwera Ine mudzamwera; ndipo ubatizo umene ndibatizidwa nao Ine, mudzabatizidwa nao;

40. koma kukhala ku dzanja langa lamanja, kapena kulamanzere sikuli kwanga kupatsa; koma kuli kwa iwo amene adawakonzeratu,

41. Ndipo pamene khumiwo anamva, anayamba kupsa mtima cifukwa ca Yakobo ndi Yohane.

42. Ndipo Yesu anawaitana, nanena nao, Mudziwa kuti iwo amene ayesedwa ambuye a mitundu ya anthu amacita ufumu pa iwo; ndipo akuru ao amacita ulamuliro pa iwo.

43. Koma mwa inu sikutero ai; kama amene ali yense afuna kukhala wamkuru mwa inu adzakhala mtumiki wanu;

44. ndipo amene ali yense afuna kukhala woyamba mwa inu adzakhala kapolo wa onse.

45. Pakuti ndithu, Mwana wa munthu sanadza kutumikiridwa, koma kutumikira, ndi kupereka moyo wace dipo la kwa anthu ambiri.

46. Ndipo iwo anafika ku Yeriko; ndipo m'mene Iye analikuturuka m'Yeriko, ndi ophunzira ace, ndi khamu lalikuru la anthu, mwana wa Timeyu, Bartimeyu, wopempha wakhungu, analikukhala pansi m'mbali mwa njira.

47. Ndipo pamene anamva kuti ndi Yesu wa ku Nazarete, anayamba kupfuula, ndi kunena, Yesu, Inu Mwana wa Davide, mundicitire ine cifundo.

48. Ndipo ambiri anamuyamula kuti atonthole: koma makamaka anapfuulitsa kuti, Inu Mwana wa Davide, mundicitire cifundo.

49. Ndipo Yesu anaima, nati, Mwitaneni. Ndipo anaitana wakhunguyo, nanena naye, Limba mtima; nyamuka, akuitana.

Werengani mutu wathunthu Marko 10