Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 9:38-43 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

38. Ndipo popeza Luda ndi pafupi pa Yopa, m'mene anamva ophunzirawo kuti Petro anali pomwepo, anamtumizira anthu awiri, namdandaulira, Musacedwa mudze kwa ife.

39. Ndipo Petro anayamuka, napita nao. M'mene anafikako, anapita naye ku cipinda ca pamwamba; ndipo amasiye onse anaimirirapo pali iye, nalira, namuonetsa maraya ndizobvala zimene Dorika adasoka, pamene anali nao pamodzi.

40. Koma Petro anawaturutsa onse, nagwada pansi, napemphera; ndipo potembenukira kumtembo anati, Tabita, uka. Ndipo anatsegula maso ace; ndipo pakuona Petro, anakhala tsonga.

41. Ndipo Petro anamgwiradzanja, namnyamutsa; ndipo m'mene adaitana oyera mtima ndi amasiye, anampereka iye wamoyo.

42. Ndipo kudadziwika ku Yopa konse: ndipo ambiri anakhulupirira Ambuye.

43. Ndipo kunali, kuti anakhala iye m'Yopa masiku ambiri ndi munthu Simoni wofufuta zikopa.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 9