Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 9:30-43 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

30. Koma m'mene abale anacidziwa, anapita naye ku Kaisareya, namtumiza acokeko kunka ku Tariso.

31. Pamenepo ndipo Mpingo wa m'Yudeya Ionse ndi Galileya ndi Samariya unali nao mtendere, nukhazikika; ndipo unayenda m'kuopa kwa Ambuye ndi m'citonthozo ca Mzimu Woyera, nucuruka.

32. Koma kunali, pakupita Petro ponse ponse, anatsikiranso kwa oyera mtima akukhalaku Luda.

33. Ndipo anapeza kumeneko munthu dzina lace Eneya, amene anagonera pamphasa zaka zisanu ndi zitatu; amene anagwidwa manjenje.

34. Ndipo Petro anati kwa iye, Eneya, Yesu Kristu akuciritsa iwe; uka, yalula mphasa yako. Ndipo anauka pomwepo.

35. Ndipo anamuona iye onse akukhala ku Luda ndi ku Sarona, natembenukira kwa Ambuye amenewa.

36. Koma m'Yopa munali wophunzira dzina lace Tabita, ndilo kunena Dorika; mkazi ameneyo anadzala ndi nchito zabwino ndi zacifundo zimene anazicita.

37. Ndipo kunali m'masiku awa, kuti anadwala iye, namwalira; ndipo atamsambitsa iye anamgoneka m'cipinda ca pamwamba.

38. Ndipo popeza Luda ndi pafupi pa Yopa, m'mene anamva ophunzirawo kuti Petro anali pomwepo, anamtumizira anthu awiri, namdandaulira, Musacedwa mudze kwa ife.

39. Ndipo Petro anayamuka, napita nao. M'mene anafikako, anapita naye ku cipinda ca pamwamba; ndipo amasiye onse anaimirirapo pali iye, nalira, namuonetsa maraya ndizobvala zimene Dorika adasoka, pamene anali nao pamodzi.

40. Koma Petro anawaturutsa onse, nagwada pansi, napemphera; ndipo potembenukira kumtembo anati, Tabita, uka. Ndipo anatsegula maso ace; ndipo pakuona Petro, anakhala tsonga.

41. Ndipo Petro anamgwiradzanja, namnyamutsa; ndipo m'mene adaitana oyera mtima ndi amasiye, anampereka iye wamoyo.

42. Ndipo kudadziwika ku Yopa konse: ndipo ambiri anakhulupirira Ambuye.

43. Ndipo kunali, kuti anakhala iye m'Yopa masiku ambiri ndi munthu Simoni wofufuta zikopa.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 9