Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 6:4-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Koma ife tidzalimbika m'kupemphera, ndi kutumikira mau.

5. Ndipo mau amene anakonda unyinji wonse; ndipo anasankha Stefano, ndiye munthu wodzala ndi cikhulupiriro ndi Mzimu Woyera, ndi Filipo, ndi Prokoro, ndi Nikanora ndi Timo, ndi Parmena, ndi Nikolao, ndiye wopinduka wa ku Antiokeya:

6. amenewo anawaika pamasopa atumwi; ndipo m'mene adapemphera, anaika manja pa iwo.

7. Ndipo mau a Mulungu anakula; ndipo ciwerengero ca akuphunzira cidacurukatu ku Yerusalemu; ndipo khamu lalikuru la ansembe linamvera cikhulupiriroco.

8. Ndipo Stefano, wodzala ndi cisomo ndi mphamvu, anacita zozizwa ndi zizindikilo zazikuru mwa anthu.

9. Koma anauka ena a iwo ocokera m'sunagoge wa Alibertino, ndi Akurenayo, ndi Aalesandreyo, ndi mwa iwo a ku Kilikiya ndi ku Asiya, natsutsana ndi Stefano.

10. Ndipo sanathe kuilaka nzeru ndi Mzimu amene analankhula naye.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 6