Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 6:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Koma masiku awo, pakucurukitsa ophunzira, kunauka cidandaulo, Aheleniste kudandaula pa Ahebri, popeza amasiye ao anaiwalika pa citumikiro ca tsiku ndi tsiku.

2. Ndipo khumi ndi awiriwo anaitana unyinji wa ophunzira, nati, Sikuyenera kuti ife tisiye mau a Mulungu ndi kutumikira podyerapo.

3. Cifukwa cace, abale, yang'anani mwa inu amuna asanu ndi awiri a mbiri yahwino, odzala ndi Mzimu ndi nzeru, amene tikawaike asunge nchito iyi.

4. Koma ife tidzalimbika m'kupemphera, ndi kutumikira mau.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 6