Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 4:29-37 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

29. Ndipo tsopano Ambuye, penyani mau ao akuopsa, ndipo patsani kwa akapolo anu alankhule mau anu ndi kulimbika mtima konse,

30. m'mene mutambasula dzanja lanu kukaciritsa; ndi kuti zizindikilo ndi zozizwa zicitidwe mwa dzina la Mwana wanu wopatulika Yesu.

31. Ndipo m'mene adapemphera iwo, panagwedezeka pamalo pamene adasonkhanirapo; ndipo anadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera, nalankhula mau a Mulungu molimbika mtima.

32. Ndipo unyinji wa iwo akukhulupira anali wa mtima umodzi ndi moyo umodzi; ndipo sananena mmodzi kuti kanthu ka cuma anali naco ndi kace ka iye yekha; koma anali nazo zonse zodyerana.

33. Ndipo atumwi anacita umboni ndi mphamvu yaikulu za kuuka kwa Ambuye Yesu; ndipo panali cisomo cacikuru pa iwo onse.

34. Pakuti mwa iwo munalibe wosowa; 1 pakuti onse amene anali nayo minda, kapena nyumba, anazigulitsa nabwera nao malonda ace a izo adazigulitsa,

35. 2 nawaika pa mapazi a atumwi; ndipo anagawira yense monga kusowakwace.

36. Ndipo Yosefe, wochedwa ndi atumwi Bamaba (ndilo losandulika mwana wa cisangalalo), Mlevi, pfuko lace la ku Kupro,

37. pokhala nao munda, anaugulitsa, nabwera nazo ndalama zace, 3 naziika pa mapazi a atumwi.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 4