Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 4:11-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Iye ndiye mwalawo woyesedwa wopanda pace ndi inu omanga nyumba, umene unayesedwa mutu wa pangondya.

12. Ndipo palibe cipulumutso mwa wina yense, pakuti palibe dzina lina pansi pa thambo la kumwamba, lopatsidwa mwa anthu, limene tiyenera kupulumutsidwanalo.

13. Koma pakuona kulimbika mtima kwa Petro ndi Yohane, ndipo pozindikira kuti ndiwo anthu osaphunzira ndi opulukira, anazizwa ndipo anawazindikira, kuti adakhala pamodzi ndi Yesu.

14. Ndipotu pakuona munthu wociritsidwayoalikuimirira pamodzi nao, analibe kanthu kakunena kotsutsa.

15. Koma pamene anawalamulira iwo acoke m'bwalo la akulu, ananena wina ndi mnzace,

16. kuti, Tidzawacitira ciani anthu awa? pakutitu caoneka kwa onse akukhala m'Yerusalemu kuti cizindikilo cozindikirika cacitidwa ndi iwo, ndipo sitingathe kukana.

17. Komatu tiwaopse asalankhulenso m'dzina ili kwa munthu ali yense, kuti cisabukenso kwa anthu.

18. Ndipo anawaitana, nawalamulira kuti asanene konse kapena kuphunzitsa m'dzina la Yesu.

19. Koma Petro ndi Yohane anayankha nati kwa iwo, Weruzani, ngati nkwabwino pamaso pa Mulungu kumvera inu koposa Mulungu;

20. pakuti sitingatheife kuleka kulankhula zimene tinaziona ndi kuzimva.

21. Koma m'mene anawaopsanso anawamasula, osapeza kanthu kakuwalanga, cifukwa ca anthu; pakuti onse analemekeza Mulungu cifukwa ca comwe cidacitika.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 4