Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 26:9-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Inedi ndinayesa ndekha, kuti kundiyenera kucita zinthu zambiri zotsutsana nalo dzina la Yesu Mnazarayo.

10. Cimenenso ndinacita m'Yerusalemu: ndipo ndinatsekera ine oyera mtima ambiri m'ndende, popeza ndidalandira ulamuliro wa kwa ansembe akulu; ndiponso pophedwa iwo, ndinabvomerezapo.

11. Ndipo ndinawalanga kawiri kawiri m'masunagoge onse, ndi kuwakakamiza anene zamwano; ndipo pakupsa mtima kwakukuru pa iwo ndinawalondalonda ndi kuwatsata ngakhale kufikira ku midzi yakunja.

12. M'menemo popita ine ku Damasiko ndi ulamuliro ndi ukumu wa kwa ansembe akulu, dzuwa lamsana,

13. ndinaona panjira, Mfumu, kuunika kocokera kumwamba kowalitsa koposa dzuwa, kunawala pondizinga ine ndi iwo akundiperekeza.

14. Ndipo pamene tidagwa pansi tonse, ndinamva mau akunena kwa ine m'cinenedwe ca Cihebri, Saulo, Saulo, undilondalonderanji Ine? nkukubvuta kutsalima pacothwikira.

15. Ndipo ndinati, Ndinu yani Mbuye? Ndipo Ambuye anati, Ine ndine Yesu amene iwe umlondalonda.

16. Komatu uka, imirira pa mapazi ako; pakuti cifukwa ca ici ndinaonekera kwa iwe, kukuika iwe ukhale mtumiki ndi mboni ya izi wandionamo Ine, ndiponso ya izi ndidzakuonekeramo we;

17. ndi kukulanditsa kwa anthu, ndi kwa amitundu, amene Ine ndikutuma kwa iwo,

18. kukawatsegulira maso ao, kuti atembenuke kucokera kumdima, kulinga kukuunika, ndi kucokera ulamuliro wa Satana kulinga kwa Mulungu, kuti alandire iwo cikhululukiro ca macimo, ndi colowa mwa iwo akuyeretsedwa ndi cikhulupiriro ca mwa Ine.

19. Potero, Mfumu Agripa, sindinakhala ine wosamvera masomphenya a Kumwamba;

20. komatu kuyambira kwa iwo a m'Damasiko, ndi a m'Yerusalemu, ndi m'dziko lonse la Yudeya, ndi kwa amitundunso ndinalalikira kuti alape, natembenukire kwa Mulungu, ndi kucita nchito zoyenera kutembenuka mtima.

21. Cifukwa ca izi Ayuda anandigwira m'Kacisi, nayesa kundipha.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 26