Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 25:23-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

23. M'mawa mwace tsono, atafika Agripa ndi Bemike ndi cifumu cacikuru, ndipo atalowa momvera milandu, pamodzi ndi akapitao akuru, ndi amuna omveka a mudziwo, ndipo pakulamulira Festo, anadza naye Paulo.

24. Ndipo Festo anati, Mfumu Agripa, ndi amuna inu nonse muli nafe pano pamodzi, muona uyu, amene unyinji wonse wa Ayuda anandiuza za iye, ku Yerusalemu ndi kunonso, ndi kupfuula kuti sayeneranso kukhala ndi moyo.

25. Koma ndinapeza ine kuti sanacita kanthu, koyenera imfa iye; ndipo popeza, iye yekha anati akaturukire kwa Augusto, ndatsimikiza mtima kumtumizako.

26. Koma ndiribe ine kanthu koti ndinenetse za iye kakulembera kwa mbuye wanga. Cifukwa cace ndamturutsira kwa inu, ndipo makamaka kwa inu, Mfumu Agripa, kuti, ndikatha kumfunsafunsa, ndikhale nako kanthu kakulembera.

27. Pakuti cindionekera copanda nzeru, potumiza wam'nsinga, wosachulanso zifukwa zoti amneneze.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 25